287 79 116MB
Chichewa Pages [184] Year 2017
Malawi Primary Education
Chichewa
T Y ED UC
AT I
O
LL RA
MO TI
ALI QU
FO
PRO
G
N
N
Buku la ophunzira la Sitandade
Adakonza ndi kusindikiza ndi a Malawi Institute of Education PO Box 50 Domasi Zomba Malawi Email: [email protected] Website: www.mie.edu.mw
© Malawi Institute of Education, 2017
Zonse za m’bukumu n’zosati munthu akopere mu njira ina iliyonse popanda chilolezo. N’zosatinso munthu achitire malonda mpang’ono pomwe. Komabe ngati munthu afuna kugwira ntchito ya zamaphunziro ndi bukuli, ayambe wapempha ndi kulandira chilolezo kuchokera kwa eni ake omwe adalisindikiza.
Kusindikiza koyamba 2017
ISBN 978-99960-44-014
Olemba Jeremiah Kamkuza
: D epartment of Inspection and Advisory Services
Foster Gama
: Malawi Institute of Education
Frackson Manyamba
: Malawi Institute of Education
Lizinet Daka
: Department of Basic Education
Wisdom Nkhoma
: Domasi College of Education
Laston Mkhaya
: Montfort Special Needs College
Benjamin David
: Blantyre Teachers’ College
Irene Kameme
: Blantyre Teachers’ College
Rex Chasweka
: Blantyre Teachers’ College
Jordan Namondwe
: Chiradzulu Teachers’ College
Luke Njovuyalema
: Lilongwe Teachers’ College
Mordky Kapesa
: Lilongwe Teachers’ College
Esther Chenjezi Chirwa
: Lilongwe Teachers’ College
Mike Rambiki
: Lilongwe Teachers’ College
Elias Chilenje
: Phalombe Teachers’ College
Adriana Mpeketula Mafunga : Phalombe Teachers’ College Owen Kazembe
: Kasungu Teachers’ College
Nicholas Kalinde
: Machinga Teachers’ College
Samson Khondiwa
: Malawi Institute of Education
Rabson Madi
: DTED
Margaret Sapili Luhanga
: Mmanga Primary School
Ryphen Chibwana
: Mmanga Primary School
Kuthokoza A Unduna wa za Maphunziro, Sayansi ndi Luso pamodzi ndi a Malawi Institute of Education akuthokoza onse omwe adathandizapo mu njira zosiyanasiyana kuyambira polemba bukuli kufika polisindikiza. Iwowa akuthokozanso kwakukulu bungwe la United States Agency for International Development (USAID) ndi United Kingdom Aid (UKAID) pothandiza ndi ndalama komanso upangiri polemba, pounika ndi kusindikiza buku la ophunzirali mogwirizana ndi Mlingo wa Boma Wounikira Maphunziro M’sukulu (National Education Standards) komanso Ndondomeko ya Boma Yokhudza Kuwerenga M’sukulu (National Reading Strategy). A Unduna wa za Maphunziro, Sayansi ndi Luso pamodzi ndi a Malawi Institute of Education akuthokozanso anthu onse omwe adaunika bukuli ndi kupereka upangiri osiyanasiyana.
Okonza bukuli Akonzi
: Max J Iphani, Peter Ngunga, Sylvester Ngoma ndi Ella Kulekana-Madambo
Ojambula Zithunzi
: Heath Kathewera, Isaiah Mphande, Richard Mwale, Henderson Mawera Raphael Mawera ndi Mphatso Phiri
Wotayipa
: Lucy Kalua-Chisambi ndi Raymond Tchuka
Woyala Mawu ndi Zithunzi : Sanderson Ndovi Mkonzi Wamkulu
: Max J Iphani
iv
Zamkatimu
Kuthokoza ............................................... iv
MUTU 1 Malonje akusukulu.................... 1
MUTU 2 nd ch....................................... 12 MUTU 3 dz ph....................................... 18 MUTU 4 mf m’b..................................... 25 MUTU 5 Kubwereza............................... 31 MUTU 6 mph nth.................................. 35 MUTU 7 tch mgw.................................. 44 MUTU 8 ng’w mch................................. 52 MUTU 9 khw phw.................................. 59 MUTU 10 Kubwereza............................... 67 MUTU 11 mg mm.................................... 71 MUTU 12 pw sh...................................... 78 MUTU 13 zw zy...................................... 85 MUTU 14 nkh ngw.................................. 92 MUTU 15 Kubwereza............................... 100 MUTU 16 mts.......................................... 104 MUTU 17 mbw......................................... 108 MUTU 18 ndw......................................... 112
MUTU 19 thw.......................................... 116 MUTU 20 Kubwereza............................... 119 MUTU 21 thy........................................... 122 MUTU 22 tsw.......................................... 126 MUTU 23 msw......................................... 130 MUTU 24 nsw.......................................... 133 MUTU 25 Kubwereza............................... 137 MUTU 26 mpw......................................... 141 MUTU 27 ntch......................................... 145 MUTU 28 nkhw........................................ 148 MUTU 29 mphw....................................... 152 MUTU 30 Kubwereza............................... 155 MUTU 31 mtch........................................ 158 MUTU 32 nthw........................................ 162 MUTU 33 mtsw........................................ 166 MUTU 34 mnkhw..................................... 170 MUTU 35 Kubwereza............................... 174
MUTU 1 Malonje akusukulu bwanji kambirana
bwino buku
Ana okonda sukulu
Malita ndi Yohane adakumana pa tsiku lotsekulira sukulu. Iwo adakambirana za maphunziro awo motere. Yohane : Uli bwanji Malita?
Malita : Ndili bwino, kaya iwe? 1
Yohane : Kodi mu Sitandade 1, mabuku owonjezera udawerengapo? Malita : Eee, ndidawerenga.
Yohane : Nanenso ndidawerengapo. Mabukuwo adali osangalatsa. Malita : Ndikhulupirira mu Sitandade 2, tikhalanso ndi mabuku ena owonjezera. Yohane : Zikatero zikhala bwino. Malita : Tiye tikalowe m’kalasi. Yohane : Tiye, Malita.
Malita ndi Yohane adali okonzeka kuwerenga mabuku owonjezera a mu Sitandade 2.
2
Ntchito
A Mafunso
1 K odi Malita ndi Yohane adakumana kuti? 2 M alita ndi Yohane adakambirana za chiyani? 3 K odi Malita ndi Yohane adasonyeza bwanji kuti ankakonda sukulu? B Kupanga ziganizo
Pangani ziganizo zomveka bwino ndi mawu awa: bwino
werenga
kambirana
kalasi
Chitsanzo
Petulo akuwerenga buku.
3
4
5
6
aA
ana
nN
nanazi
iI
insa
mM
mango
uU
uta 7
kK
kalulu
oO
ovololo
lL
lalanje
eE
emvulopu
wW
wailesi 8
tT
tebulo
dD
diso
sS
sefa
pP
poto
nd
ndalama 9
ch
chule
yY
yala
bB
buku
zZ
zala
gG
galu 10
rR
lira
fF
fulu
hH
hamala
jJ
jombo
vV
vava 11
MUTU 2
nd ch
kwe mwi
nso mlu
bwa
nd nda ndo ndi ndu nde ndodo
ndalama
ndiwo
mitundu
12
ndowa
Dimba la a Ndelemani
A Ndelemani anyamula ndowa ziwiri. Iwo aika ndowa kundodo. Ndowazo ndi zamitundu yosiyana. A Ndelemani amathirira kabichi m’dimba mwawo. Alendo ambiri amachita chidwi ndi dimbali. A Ndelemani amapeza ndalama zochuluka akagulitsa kabichi wawo. 13
Ntchito
A Mafunso
1 Kodi a Ndelemani anyamula chiyani? 2 K odi a Ndelemani amapeza chiyani akagulitsa kabichi? 3 M ukuganiza ndi chifukwa chiyani a Ndelemani amathirira kabichi wawo? B Kupanga mawu
Pangani mawu poika nd m’mipata. Chitsanzo ___olo ndolo 1 __owa 2 __ere 3 __iwo 4 __ani 5 __ulu 14
ndo
mba
le
thi
mu
ch che cho cha chu chi chala
chiswe
chimanga
chidole
15
chulu
Chiswe chiluma Chikondi
Chikondi ndi mwana wa a Chekani. Iye amakhala ku Chongoni. Tsiku lina Chikondi anapita pachulu kuti akatenge dongo. Iye amafuna kuumba chidole. Akutenga dongolo, chiswe chachikulu chinamuluma. Chiswecho chinaluma chala chake chaching’ono. Iye analira chifukwa cha ululu. 16
Ntchito
A Mafunso
1 Kodi Chikondi ndi mwana wa yani? 2 Ndi chifukwa chiyani Chikondi anakatenga dongo? 3 Ndi chifukwa chiyani Chikondi anakatenga dongo la pachulu? B Kulemba mawu
Lembani mawu kuchokera mu mabokosi otsatirawa: Chitsanzo
cho
yo
che
la
Mawu: chola, cheyo chi na cho
swe
chu
la
cha
lu 17
MUTU 3
dz ph
chu ndi
ngo kwa
swe
dz dza dzi dzu dze dzo madzi
dzombe
dzinja
dzuwa
18
udzu
Tadala aona dzombe Inali nyengo yadzinja dzuwa litatuluka. Tadala ankapita kumjigo kukatunga madzi. Madziwo anali woti asambe popita kusukulu. Asanafike kumjigoko, Tadala anaona dzombe. Dzombe lambiri linatera mu udzu.
19
Tadala anabwerera kumudzi mofulumira. Iye anakauza makolo ake za dzombelo. Makolowo anapita kukatola dzombe. Iwo amakonda kudya dzombe.
Ntchito
A Mafunso 1 Kodi Tadala amakatunga madzi kuti? 2 Kodi Tadala anaona chiyani pokatunga madzi? 3 Mukuganiza ndi chifukwa chiyani Tadala anakauza makolo ake za dzombe?
20
B K upeza mawu amene ali ndi dz
Tsekani mzere kunsi kwa mawu amene ali ndi dz. Chitsanzo
Iye akudya dzungu. Iye akudya dzungu.
1 Ana akuothera dzuwa. 2 Atate atola dzombe. 3 Mudzi uli pafupi ndi nyanja.
21
dya mbe
dzi nga
go
ph phi pha phu pho phe phika
phiri
phoso
phokoso
22
phazi
Mwana wokonda maphunziro Eliza amakhala mu dera la Phanga. Derali lili pafupi ndi phiri. Iye amaphunzira pa sukulu ya Phanga. Amavala nsapato zansalu. Nsapatozo ndi zolingana ndi phazi lake. Popita kusukulu, iye amatenga phoso. Phosoli amaphika ndi makolo ake. Eliza sachita phokoso pophunzira. Iye amakonda maphunziro a Chichewa, Chingerezi ndi masamu. Aphunzitsi amamukonda chifukwa ndi mwana womvera. 23
Ntchito
A Mafunso
1 Kodi Eliza amaphunzira kuti? 2 Ndi chifukwa chiyani aphunzitsi amakonda Eliza? 3 Kodi muzichita chiyani kuti aphunzitsi azikukondani? B Kupanga mawu
Pangani mawu poika phi phe pha pho m’mipata. Chitsanzo __wa
phewa 1 __ so 2 __ la 3 __ ri 24
MUTU 4
mf
m’b
phu nda phi che
wo
mf mfa mfo mfi mfu mfe mfolo
mfumu
imfa
25
mfundo
Kulandira chimanga
Mfumu Chidothi idaitanitsa makolo omwe adachita nawo chitukuko cholambula msewu. Iyo idafuna kuti alandire chimanga. Mfumu idauza makolo onse kuti akhale pamfolo. Iyo simafuna kuti pakhale chisokonezo. Makolowo adasangalala ndi mfundo imeneyi. Chisokonezo chikhoza kubweretsa imfa. Kumwambowu kudali asirikali andodo. Iwo amakhazikitsa bata. 26
Ntchito
A Mafunso
1 Kodi adaitanitsa makolo ndani? 2 Ndi chifukwa chiyani makolowo adaitanidwa? 3 Ndi chifukwa chiyani makolo adasangalala ndi mfundo yokhala pamfolo? B Kupeza mawu omwe ali ndi mf
Pezani mawu amene ali ndi mf m’ziganizo zotsatirazi. Chitsanzo
Mfumu yakhala pa mpando. Mfumu yakhala pa mpando.
1 Makolo ali pamfolo. 2 Mfumu inatenga ndodo. 3 Iye adanena mfundo yabwino. 27
kha dzo
chi mfu
nse
m’b m’be m’bu m’bo m’ba m’bi m’bobo
m’bale
m’bawa
m’bandakucha
28
m’busa
Jenifa ndi m’bale wake
Tsiku lina Jenifa ndi m’bale wake adali paulendo. Iwo ankapita kumalo wosungirako nyama. Bambo awo omwe ndi m’busa adawaperekeza. Iwo adanyamuka m’bandakucha. Atafika kumaloko adaona njoka ya m’bobo. Njokayo idali mu mtengo wa m’bawa. Iwo adaopa kufika pafupi ndi m’bawawo. Bambo awo adawauza kuti m’bobo ukaluma umapha. Jenifa ndi m’bale wake adayenda molambalala m’bawa uja. 29
Ntchito
A Mafunso
1 Kodi Jenifa ndi m’bale wake ankapita kuti? 2 Njoka ya m’bobo idali kuti? 3 Mukanakhala inu, mukanatani mutaona m’bobo? B Kufananitsa mawu
Pezani mawu mu B ofanana ndi omwe ali mu A. Chitsanzo
A 1 m’bobo
B 2 m’bobo
A
B
1 m’bobo
1 m’bawa
2 m’bale
2 m’bobo
3 m’bandakucha
3 m’bale
4 m’bawa
4 m’bandakucha 30
MUTU 5 Kubwereza 1 T chulani liwu loyamba lopezeka mu mayina a zinthu zomwe zili mu mabokosiwa. Chithunzi choyamba mutu 3
Chithunzi choyamba mutu 2
31
2 T chulani maliwu a malembo kuchokera mu mabokosiwa.
dz
m’b
mf
ch
nd
ph
3 W erengani maphatikizo otsatirawa. nda
phu
chi
cho
chu
nde
pha
m’bu
m’ba
dze
m’bo
ndi
phe
m’bi
cha
dza
32
4 Werengani mawu otsatirawa. ndalama
m’bebe
mudzi
chule
dzana
ndodo
mfumu
m’bobo
phunzira
chimfine m’banga phiri
phokoso
chala
dzulo
chipatala
ndulu
phika
chake
ndiwo
chatupa
ndolo
dzira
mfolo
5 Werengani nkhani yotsatirayi. Amanga nyumba m’tauni
Makolo a Yamikani adapeza ndalama. Iwo adagula malo m’tauni. Mfumu ya deralo idachitira umboni pogula malowo. Malowo adali pafupi ndi chipatala. Iwo adamanga nyumba pamalopo. Makolowo adabzala
33
mitengo ya m’bawa. Masiku ambiri ankamva phokoso kuchokera kuchipatala. Mafunso
1 Kodi nyumba ya makolo a Yamikani adaimanga kuti? 2 Ndani adachitira umboni pogula malo? 3 Mukuganiza ndi chifukwa chiyani makolo a Yamikani adagula malo m’tauni?
34
MUTU 6 phi
mph nth mfu
dzo mba
che
mph mpha mpho mphi mphu mphe mphuno
mphongo
mphiri
mphamba
35
mphaka
Chisomo ndi Mphatso
Chisomo ndi Mphatso amaphunzira pasukulu ya Mphako. Tsiku lina
36
akupita kusukulu anaona mphaka. Iwo anakambirana motere. Chisomo : Kodi wamuona mphaka?
Mphatso : Eee, ndamuona. Akuoneka wokongola ngati wanga. Chisomo : Uli ndi mphaka?
Mphatso : Eee, ndili naye wamphongo. Chisomo : Kodi amakonda kutani? Mphatso : Amakonda kugona pamphasa.
Chisomo : Mphakayo amadya chiyani?
Mphatso : Iye amadya mpheta, mphamba ndi mphemvu. Chisomo : Kodi amazigwira bwanji? Mphatso : Iye amazidumphira.
Chisomo : Kodi ndi wamphamvu?
Mphatso : Eee! Dzulo anagwira njoka ya mphiri. 37
Chisomo : Ndiye siinamulume?
Mphatso : Inamuluma pamphuno ndi pamphumi koma anaipha. Chisomo ndi Mphatso anafika kusukulu ndipo analowa m’kalasi.
Ntchito
A Mafunso 1 Ndani anali ndi mphaka wamphongo? 2 Kodi mphakayo anagwira njoka yanji? 3 Mukuganiza ndi chifukwa chiyani mphaka amakonda kugona pamphasa?
38
B Kufananitsa zithunzi ndi mayina Fananitsani zithunzi zotsatirazi ndi mayina ake pogwiritsa ntchito manambala. Chitsanzo
1
1
mphaka
mphamba
2
mphasa
3
mphaka
4
mphemvu
39
mwe ngo mpha dzu ndi
nth ntha nthe ntho nthu nthi
nthenda
nthudza
nthanda
nthiwatiwa
40
nthenga
Nthano ya nthiwatiwa
Agogo anga a Nthenda adatiuza nthano. Iwo adati padali munthu dzina lake Khama. Iye adapita kuthengo kuti akadye nthudza. Khama akuyenda, adaona chinthu chokongola. Chinthucho chidali nthenga ya nthiwatiwa. Khamayo adafunafuna nthiwatiwayo. Ataiona adafuna 41
kuigwira kuti akaiwete. Nthiwatiwa idachita mantha ndipo idathawa. Iye adaithamangitsa mpaka adatopa. Khama adabwerera kumudzi modandaula. Iye adalingalira za nthiwatiwa mpaka nthanda idaoneka. Khama adadziwa kuti kwacha.
Ntchito
A Mafunso 1 Tchulani dzina la agogo amene adafotokoza nthano. 2 Kodi Khama adathamangitsa chiyani kuthengoko? 3 Kodi mukadatani mukadaona kuti kwada?
42
B Kusankha mawu okhala ndi nth Sankhani mawu omwe ali ndi nth mu ziganizo zotsatirazi. Chitsanzo Nthiwatiwa imathamanga kwambiri. Nthiwatiwa imathamanga kwambiri. 1 Iye anatola nthenga kuthengo. 2 Nthanda ndi nyenyezi. 3 Nthudza zimakoma.
43
MUTU 7
tch mgw
dza nthu the cho gwi
tch tcha tchi tchu tche tcho tchetcha
tcheru
tchalitchi
tchena
44
matchona
Matchona a ku Joni
Kalekale anthu ena ankapita ku Joni. Iwo ankayenda ulendo wapansi. Nthawi zina kukawadera ankagona patchire. Anthuwo ankagona mwatcheru kuopa zilombo zolusa. Iwo ankatchetcha patchirepo asanagone.
45
Anthu ambiri ankakhalitsa ku Joni. Iwo ankasanduka matchona. Amene ankabwerako ankavala bwino. Iwo ankatchena ngati akupita ku ukwati. Ambiri ankatchuka chifukwa cha kutchenako.
Ntchito
A Mafunso 1 Kodi kalekale anthu ankapita kuti? 2 Kodi anthu ankagoneranji mwatcheru patchire? 3 Mukuganiza kuti ndi chifukwa chiyani anthu ankayenda pansi popita ku Joni?
46
B Kufananitsa ziganizo Sankhani ziganizo za mu B zomwe zikufanana ndi za mu A. Chitsanzo
A 1 ndi B 2 1 2 3 4
A I wo agona patchire. A kupita kutchalitchi. Litchowa lasowa. S ukuluyi ndi yotchuka.
47
1 2 3 4
B Litchowa lasowa. I wo agona patchire. S ukuluyi ndi yotchuka. A kupita kutchalitchi.
bwe ndu tcho mwa bwi
mgw mgwa mgwe mgwi
mgwere
mgwalangwa
mgwazo
mgwirizano
48
Kusamalira mitengo
M’mudzi mwa a Kalima muli mitengo yosiyanasiyana. Ina mwa mitengoyo ndi mgwalangwa, m’bawa ndi mvunguti. Anthu am’mudzimo amasamalira mitengoyo mwamgwirizano. Iwo sadula mitengoyi mwachisawawa. Chaka chilichonse anthuwo amakumba mgwere waukulu. 49
Anthu ena amakumba mgwere mwamgwazo. Mgwerewo umatchinga madzi osefukira kuti asagwetse mitengoyo.
Ntchito
A Mafunso 1 Tchulani mitengo yomwe amaisamalira m’mudzi mwa a Kalima. 2 Ndi chifukwa chiyani anthu amakumba mgwere? 3 Fotokozani ubwino wosamalira mitengo.
50
B Kutsiriza ziganizo Tsirizani ziganizo poika mawu awa: mgwere, mgwirizano, mgwazo ndi mgwalangwa mu mipata yoyenera. Chitsanzo Anthu akukumba _______. Anthu akukumba mgwere. 1 Mtengo wa ________ ndi wautali. 2 Iye amagwira ntchito mwa______. 3 M________ ndi wofunika m’kalasi.
51
MUTU 8
ng’w mch
mgwe mvu mba ngo tchi
ng'w ng'wi ng'wa ng'we nyang’wa
zing'wenyeng'wenye
ng’waa
kang’wing’wi
52
Madyerero aufumu
Tsiku lina mu dera la a Nyang’wa munali madyerero aufumu. Kunali magule osiyanasiyana monga gule wamkulu, chimtali ndi honala. Akang’wing’wi anali komweko. Mfumu Nyang’wa inanyang’wadi monga mwa dzina lake. Amayi ndi abambo ng’oma ndi zing’wenyeng’wenye mwaluso. 53
Aliyense anavina monyang’wa. Mudzi wonse wa Nyang’wa unali teketeke.
Ntchito
A Mafunso 1 Kodi madyerero aufumu anachitikira kuti? 2 Tchulani magule atatu omwe anthu anavina pa mwambowu. 3 Fotokozani kufunika kwa magule pa mwambo waufumu.
54
B Kupanga mawu Pangani mawu poika maphatikizo awa: ng’wa, ng’we ndi ng’wi mu mipata yoyenera. Chitsanzo
nya________ nyang’wa
1 kang’wi______ 2 monya_______ 3 zi____nyeng’wenye
55
mku mwe nga ng’wi ng’o
mch mcha mchi mchu mche mcho mchimwene
mcheni
mchewere
mchikumbe
56
mchere
Mchikumbe waphindu
Chisomo ali ndi mchimwene wake Kamchacha. Kamchacha amakhala ku Mchezi. Iye ndi mchikumbe. Kamchacha amalima mbewu zosiyanasiyana. Zina mwa mbewuzo ndi mchewere, mapira ndi chimanga. Iye amawetanso nsomba monga mcheni, chambo ndi milamba.
57
Mchewere ndi mapira amagulitsa. Chimanga amadya ndi banja lake. Kamchacha alinso ndi golosale. Amagulitsa mchere, shuga ndi sopo. Anthu ambiri amadzagula mchere m’golosalemo.
Ntchito
A Mafunso
1 Tchulani dzina la mchimwene wake wa Chisomo. 2 Kodi mchimwene wake wa Chisomo amaweta nsomba zamtundu wanji? 3 Mukuganiza kuti Kamchacha anachita chiyani kuti akhale ndi golosale? B Kupeza mawu omwe ali ndi mch Pezani mawu atatu omwe ali ndi mch kuchokera mu nkhani ya “Mchikumbe waphindu.” Chitsanzo mchimwene 58
MUTU 9
khw phw
mchi nso shu tsa bwe
khw khwa
khwi
khwe
khwakhwawe
khwima
khwasula
khwanya
59
khwekhwe
Khwakhwawe akodwa pa khwekhwe
Idali nthawi yadzinja. Chimanga chidali chisadakhwime. Ndiwo zamasamba zidali ponseponse. Chimwemwe adatopa ndi kudyera khwanya. Iye adauza atate ake kuti akufuna kukhwasula. Atate akewo adatchera khwekhwe. Chimwemwe adasangalala kuti akhwasula. 60
Tsiku lotsatira, atatewo adapita kokazonda khwekhwelo. Atafika, adaimba likhweru kuitana Chimwemwe. Iye adathamangira komwe adatchera khwekhwelo. Zachisoni, iwo adapeza khwakhwawe. Khwakhwawe ndi chibuluzi chachikulu. Atate adamuonjola khwakhwawe uja modandaula. Khwakhwaweyo adathawa.
Ntchito
A Mafunso 1 Ndani adatchera khwekhwe? 2 Kodi Chimwemwe adatopa ndikudyera chiyani? 3 Mukuganiza kuti ndi chifukwa chiyani atate adaonjola khwakhwawe modandaula?
61
B Kupanga mawu Pangani mawu poika khwa, khwe kapena khwi mu mipata yoyenera. Chitsanzo ____khwawe khwakhwawe 1 ___ nya 2 ___ ma 3 ___ khwe
62
khwa tche njo ndi su
phw phwa
phwi
phwetekere phwanyika
63
phwe
iphwa chithaphwi phweka
A Chiphwafu akonza njinga A Chiphwafu adali pa ulendo wochokera kumsika. Kumsikako adagula phwetekere ndi nyama. Ali panjira, tayala la njinga yawo lidaphwa. A Chiphwafu adakhotera pachithaphwi. Iwo adachotsa
64
chubu mutayala. Adapopa chubucho ndi kuchinyika pachithaphwipo. Iwo adafuna kuona pomwe padabooka. Atakonza adapitiriza ulendo wawo. Iwo adasangalala popeza phwetekere wawo sadaphwanyike.
Ntchito
A Mafunso 1 Kodi a Chiphwafu ankachokera kuti? 2 Kodi a Chiphwafu adasangalala chifukwa chiyani? 3 Ndi chifukwa chiyani a Chiphwafu sadavutike pokonza njinga yawo?
65
B Kukonza mawu olakwika Konzani mawu otsatirawa omwe alembedwa molakwika. Chitsanzo pwanya phwanya 1 pwiti 2 pwetekere 3 pwete
66
MUTU 10 Kubwereza 1 Tchulani liwu loyamba lopezeka mu mayina a zinthu zomwe zili mu mabokosiwa.
67
2 Tchulani maliwu a malembo kuchokera mu mabokosiwa. mph
nth
tch
mgw
ng’w
mch
khw
phw
3 Werengani maphatikizo otsatirawa. mpho nthe
tchu
mgwa
ng’wi mche
khwe
phwe
mphu mgwe
mcho
ng’wa
khwi
phwi
mchu
tcho
68
4 Werengani mawu otsatirawa. mphamba
nthiwatiwa
mphemvu
tcheru
mgwere
nyang’wa
mcheni
khwangwala
nthudza
tchire
kang’wing’wi
khwanya
mphaka
mchikumbe
mgwidyo
69
5 Werengani nkhani yotsatirayi.
Mphaka ndi khwakhwawe
Kalekale kudali mchikumbe wina dzina lake Kalulu. Iye adali ndi anyamata awiri, Mphaka ndi Khwakhwawe. Iwo ankalima mbewu monga mchewere, phwetekere ndi chimanga. Mchikumbeyo adali wotchuka mu deralo. Iye ankakonda Mphaka chifukwa ankalimbikira kulima. Mphaka adayamba kudya zakudya zabwino za mchikumbeyu. Khwakhwawe adamuthamangitsa chifukwa cha ulesi. Kuyambira pomwepo, Khwakhwawe amakhala kuphanga. Mafunso 1 Tchulani dzina la mchikumbe. 2 Kodi Mphaka ndi Khwakhwawe ankagwira ntchito yanji kwa mchikumbe? 3 Kodi mu nkhaniyi mwaphunziramo chiyani? 70
MUTU 11 m g
mm
mgwi mche mpha tchu cho
mg mgi mge mga mgo mgu mganda
mgaiwa
mgugu
mgonero
71
mgolo
Tsiku laukwati
Tsiku laukwati kwathu Ndi tsiku lachisangalalo zedi Amayi amakonzekera kwambiri Iwo amagayitsa mgaiwa Mgaiwa amaphikira thobwa Thobwalo amaliphika mu mgolo Tsiku laukwati kwathu Ndi tsiku lachisangalalo kwambiri Abambo amavina mganda Mganda ndi gule wosangalatsa Povina pamamveka mgugu Akavina amadya mgonero 72
Ntchito
A Mafunso
1 Kodi pokonzekera tsiku laukwati amayi amatani? 2 Kodi thobwa la pa ukwati amaliphika mu chiyani? 3 Mukuganiza ndi chifukwa chiyani anthu amavina magule pa ukwati? B Kupanga mawu
Pangani mawu oyenera kuchokera mu mabokosi potsatira chitsanzo ichi. mgo
nda
mga
lo
Mawu: mgolo, mganda mgu di mgo
gu
mga
nero
mgo
iwa 73
mge mbo
mfu mgi
dza
mm mmo mme mmu mmi mma
mmodzi
mmera
mmene
mmemo
74
mmisiri
Mmisiri waluso
M’mudzi mwa a Pindani muli nyumba yokongola kwambiri. Nyumbayi adamanga ndi mmisiri wamkazi, mmisiri dzina lake anali Zione Patani. Mmisiriyu ankamanga mwamsanga ndi mwaluso.
75
Mmisiriyu ali ndi mwana mmodzi. Iye ndi mwana wake ankakondanso kulima. M’munda mwawo munkakhala mmera wobiriwira zedi.
Ntchito
A Mafunso 1 Tchulani mudzi womwe mmisiri wamkazi ankakhala. 2 Kodi mmisiriyu ankagwira ntchito yanji? 3 Kodi inu mumafuna kudzagwira ntchito yanji?
76
B Kulemba lembo lalikulu
Lembani lembo lalikulu koyambirira kwa ziganizo zotsatirazi. Chitsanzo
madalitso amakonda kulima. Madalitso amakonda kulima. 1 mmisiri wathu ndi waluso. 2 iye ali ndi mwana mmodzi. 3 tonse timakonda kulima.
77
MUTU 12 pw
sh
mgo mka mme nyu dzi
pw pwi pwa pwe zipwete
pweteka
pwepwete
pwatapwata
78
pwayi
Zipwete zokoma
Tamanda amakonda zipwete. Zipwete zimakoma kwambiri. Tsiku lina Tamanda ndi anzake analowa m’munda. Iwo amafuna zipwete. Akufuna zipwetezo, anaona pwayi. Pwayiyo anatera pa chipwete. Iwo sanaope. Mwamwayi, anapeza zipwete zambiri. 79
Iwo anabwerera kumudzi ali osangalala. Atangofika, mvula inayamba kugwa pwatapwata. Tamanda ndi anzake anayang’anizana naseka pwepwete chifukwa sananyowe.
Ntchito
A Mafunso 1 Kodi Tamanda ankakonda chiyani? 2 Ndi chifukwa chiyani Tamanda ndi anzake anaseka pwepwete? 3 Kodi chikanachitika ndi chiyani mvula ikanawapeza panjira anawo?
80
B Kufananitsa zithunzi ndi mayina Fananitsani zithunzi zotsatirazi ndi mayina ake pogwiritsa ntchito manambala. Chitsanzo
1 pwepwete
1 pwepwete
2 zipwete
3 pwayi
4 pweteka
81
pwa mvu nza dzi
nyo
sh sho
she
sha
shati
shuga
shasha
shisha
82
shu
shosha
shi
Banja la a Shawa
Shila ndi mwana wa a Shawa. A Shawa amakonza mawailesi ndi mafoni. Akapeza ndalama, a Shawa amagula shuga ndi buledi. Shila amakonda phala lothira shuga. Shuga amazunitsa phala. Shila akadya phala lothira shuga, amasewera osatopa mwamsanga.
83
Tsiku lina Shila ndi amayi ake anapita kumsika. Kumsikako anagula chitenje, diresi ndi shati. Shatiyo inali ya abambo. A Shawa anaikonda shatiyo.
Ntchito
A Mafunso 1 Kodi Shila ndi mwana wa yani? 2 Ndi chifukwa chiyani Shila amakonda phala lothira shuga? 3 Ndi chifukwa chiyani a Shawa anasangalala ndi shati? B Kupeza mawu omwe ali ndi sh
Pezani mawu omwe ali ndi sh kuchokera mu nkhani yomwe mwawerenga. Chitsanzo
Mawu: Shawa
84
MUTU 13 nje
zw msi
zy
sha
gu
yo
zw zwi zwe zwa zweta
zwee
chizwezwe
zizwa
85
zizwitsa
Kuipa kwa chamba
Tsiku lina Chisomo ndi Dalo anacheza ndi mphunzitsi wawo motere. Mphunzitsi : Kodi ana inu munamvera wailesi dzulo? Chisomo
: Ayi, kodi amakamba zotani?
Mphunzitsi : Amakamba zoti chamba chimachititsa chizwezwe. Dalo
: Chizwezwe? 86
Mphunzitsi : Ee, wozweta mutu amazizwitsa. Chisomo
: Amazizwitsa bwanji?
Dalo
: Kusuta chamba ndi koipa, eti?
Mphunzitsi : Amadya zotoleza kudzala.
Mphunzitsi : Ee. Pewani kusuta chamba kuti mupewe kuchita chizwezwe. Chisomo
: Tamva aphunzitsi. Kusuta chamba si kwabwino. Chisomo ndi Dalo anabwerera kunyumba atazindikira za kuipa kosuta chamba.
Ntchito
A Mafunso 1 Kodi mphunzitsi amacheza ndi yani? 2 Ndi chifukwa chiyani kusuta chamba kuli koipa? 3 Kodi inu mungatani mutaona anzanu akusuta chamba? 87
B K ulemba mzere kunsi kwa zw m’mawu Lembani mzere kunsi kwa zw mu mawu omwe ali m’munsiwa. Chitsanzo zwee zwee 1 kuzweta 2 zizwitsa 3 chizwezwe
88
zwe
dzu
mva
zo
chi
zy zye
zyi
zyu
zya
zyoli
zyolika
zyolizyoli
kazyozyo
89
zyo
Chifundo m’kalasi
M’mudzi mwa a Kazyozyo mudali mnyamata dzina lake Chifundo. Iye ankaphunzira pa sukulu ya Maziko. Nthawi zambiri aphunzitsi akamuyandikira, iye ankangozyolika. Tsiku lina aphunzitsi ake adamuitanira pambali ndipo adayankhulana motere. Mphunzitsi : N’chifukwa chiyani umakhala zyolizyoli? Chifundo : Palibe aphunzitsi. Mphunzitsi : Chifundo usaope. Fotokoza vuto lako.
90
Chifundo
: Kungoti ndilibe cholembera.
Chifundo
: Zikomo aphunzitsi.
Mphunzitsi : Ukanandiuza. Kwaya cholembera ichi.
Ntchito
A Mafunso
1 Kodi Chifundo ankachokera m’mudzi mwa yani? 2 Tchulani dzina la sukulu yomwe Chifundo ankaphunzirapo. 3 Kodi inu mungatani mutakhala kuti mulibe cholembera? B K upanga mawu Pangani mawu poika zy m’mipata. Chitsanzo __oli zyoli 1 __olika 2 ka__ozyo 3 __oli__oli 91
MUTU 14 nkh zyo phu
tsi
ngw mwe
kwa
nkh nkhe nkho nkha nkhu nkhi nkhumba
nkhosa
nkhanga
nkhuli
92
Ziweto za a Nankhoma
A Nankhoma amakhala mu dera la Liwonde. Iwo amaweta nkhuku, nkhunda, nkhanga, nkhosa ndi nkhumba. Nkhuku zimayendera limodzi ndi nkhanga pokadya kudzala.
93
A Nankhoma amakazinga nyama ya nkhuku, nkhunda ndi nkhanga pafupipafupi. Iwo amachita izi chifukwa cha nkhuli. A Nankhoma amagulitsa nkhumba ndi nkhosa kuti apeze ndalama. Ndalamazo amalipirira ana sukulu.
Ntchito
A Mafunso
1 Tchulani ziweto ziwiri zomwe a Nankhoma amaweta. 2 Ndi chifukwa chiyani a Nankhoma amakazinga nyama pafupipafupi? 3 Kodi inu mutakhala mlimi, mungawete ziweto zanji?
94
B Kutsiriza ziganizo
Tsirizani ziganizo polemba mawu awa: nkhunda, nkhuli, nkhosa ndi nkhanga mu mipata yoyenera. Chitsanzo
Nyama ya _____ ndi yofewa kwambiri. Nyama ya nkhosa ndi yofewa kwambiri. 1 _____ imafanana ndi njiwa. 2 _____ ili ndi mawanga. 3 A Nankhoma ali ndi _____.
95
nkho
nga
zi
pe
ngw ngwe
ngwi
ngwa
ngwazi
nsungwi
chinangwa
ngwere
96
lu
Ngwazi ya masamu
Wanangwa amakhala mu mzinda wa Lilongwe. Iye ali ndi anzake awiri, Sangwani ndi Ulemu. Onsewa amaphunzira pa sukulu ya Ngwangwa. Pa Ngwangwa pali nsungwi zambiri. Wanangwa ndi anzake amatenga chinangwa akamapita kusukulu. Wanangwa ndi wanzeru. Iye ndi 97
ngwazi pa phunziro la masamu. Iye amaphunzitsa anzake masamu. Aphunzitsi anamkonzera ulendo wopita kunyanja. Iye anakaona mvuwu m’madzi ndi ngwere pamchenga.
Ntchito
A Mafunso
1 Tchulani mayina atatu a ophunzira a pa sukulu ya Ngwangwa. 2 Kodi Wanangwa amatenga chakudya chanji popita kusukulu? 3 Mukuganiza ndi chifukwa chiyani ophunzira amayenera kuthandizana mu kalasi?
98
B Kupanga ziganizo Pangani ziganizo ndi mawu awa: chinangwa, chingwe, ngwazi ndi nsungwi. Chitsanzo Chilenje ndi ngwazi ya Chichewa.
99
MUTU 15 Kubwereza 1 Tchulani liwu loyamba lopezeka mu mayina a zinthu zomwe zili mu mabokosiwa.
100
2 Tchulani maliwu a malembo omwe ali mu mabokosiwa. mg
sh
zw
mm
ngw
pw
zy
nkh
3 Werengani maphatikizo otsatirawa. mga
shu
zwi
mmo
zye
ngwi
pwa
zyo
nkha
ngwe
sha
mmi
pwe
mgu
zwee
nkho
101
4 Werengani mawu otsatirawa. pwayi
mmisiri shuga
chipwirikiti mgolo
nkhumba
ngwangwa zizwitsa
nkhuku
mmera zipwete
shati
zweta
mganda nkhosa
ngwazi
5 Werengani nkhani yotsatirayi. Chipwirikiti pa ukwati
Pamudzi pa a Ngwangwa padali madyerero aukwati. Kudali zakudya ndi zakumwa zosiyanasiyana. Kudali ndiwo monga nyama ya nkhuku, nkhosa ndi nkhanga. Ena adavina mganda. Shasha wina adaba poto wa nyama ya nkhuku. Iye adachoka pamalopo mozemba. Adangoti khonde zwee.
102
Mayi wina adazizwa ndi mayendedwe ake. Mayiyo adakuwa. Padali chipwirikiti. Abambo ena adamugwira. Atamufunsa, iye adangoti zyoli.
Ntchito Mafunso
1 Kodi madyerero adachitikira kuti? 2 Kodi pa ukwatiwu padali ndiwo zanji? 3 Fotokozani kuipa kwa kuba.
103
MUTU 16
mts
nkhu gwi zwe
zyo
mga
mts mtse mtsu mtsa mtso mtsi mtsuko
mtsinje
mtsutso
mtsitsi
104
mtsetse
Ana abwino Ana abwino
Likangolira beru, ngo! Aphunzitsi m’kalasi n’kuwatulutsa Liwiro wakunyumba layambika Akathandize makolo pakhomo
105
Ana abwino Mokondwera ayenda pa mtsetse Mtsuko pamutu, chigubu m’manja Ulendo wa ku mtsinje Ana abwino Pofika amayi awalandira madzi Mokondwera awiritsa m’chidebe Amwe aukhondo madzi
Ntchito
A Mafunso
1 Perekani ntchito imodzi yomwe ana amagwira. 2 Tchulani ziwiya zomwe zili mu ndakatuloyi. 3 Fotokozani njira ina yosamalira madzi kuti akhale aukhondo.
106
B Kutsiriza ziganizo Tsirizani ziganizo poika mawu awa: mtsuko, mtsinje, mtsetse ndi mtsikana m’mipata yoyenera. Chitsanzo
Maliya ndi ________ wanzeru. Maliya ndi mtsikana wanzeru. 1 Amayi asenza ______ popita kumadzi. 2 Njinga imathamanga pa ______. 3 Anyamata akusambira mu ______ .
107
MUTU 17 mtse
mbw nya
dzi
kho
nza
mbw mbwe mbwa mbwi mbwanda mbwadza
tambwali tumbwa
108
mbwita
Luka ambwita
Padali mnyamata wina dzina lake Luka. Iye ankakonda kuonjola nyama mu misampha ya anzake. Tsiku lina Luka adaona mbwadza. Iye adapeza kalulu atakodwa. Pamene ankafuna kumuonjola, msampha udaduka. Adalumpha kuti ambwandire kaluluyo. Mwatsoka
109
adambwita ndi kugwera pamsamphapo. Luka adavulala kwambiri. Kalulu adathawa. Mtedza wapamsamphapo udangoti mbwee. Mwini msampha adamupeza. Iye adamuyankhula motumbwa kuti wapeza polekera. Luka adakadyera mbwanda. Iye adati sadzabanso.
Ntchito
A Mafunso
1 Tchulani dzina la mnyamata mu nkhaniyi. 2 Ndi chifukwa chiyani kalulu adathawa? 3 Fotokozani kuipa kwa kuba.
110
B Ndagi/zilapi Perekani matanthauzo a ndagi/zilapi zotsatirazi. Chitsanzo
Bokosi langa lotsekula ndi chala.
Yankho
mtedza
1 Zungulira uku tikumane uku. 2 Chimunda uko pokolola n’kumanja. 3 Phiri lakwathu lokwera ndi ana omwe.
111
MUTU 18
ndw
mpha mbwi gwe nkhu njo
ndw ndwa
ndwi
kondwa
nkhandwe
tsindwi
chikondwerero
112
ndwe
Nkhandwe ilowa m’mudzi Tsiku lina nkhandwe idalowa m’mudzi mwa Gondwa. Iyo idaona nkhuku pakhonde. Nkhandweyi idaganiza kuti ikapha nkhukuyo pakhala chikondwerero.
Nkhandwe idalumphira nkhukuyo. Nkhuku ija idaulukira pa tsindwi la nyumba. Tsindwili lidali losasuka. 113
Nkhukuyo idagwera m’nyumba. Nkhandwe sidakondwe. Iyo idabwerera kutchire. Maganizo achikondwerero adathera pomwepo.
Ntchito
A Mafunso
1 Nkhandwe idalowa m’mudzi mwa yani? 2 Tchulani komwe nkhandwe idapita italephera kugwira nkhuku. 3 Mukuganiza kuti tsindwi la nyumba lidasasuka ndi chiyani?
114
B Kutsiriza ziganizo Tsirizani ziganizo poika mawu oyenera m’mipata kuchokera m’mikutiramawu. Chitsanzo
Atate adapita ku ________ (kondwa, chikondwerero). Atate adapita ku chikondwerero. 1 Nkhuku yaulukira pa _______ (tsindwi, nkhandwe). 2 Usiku kunali mphepo ya ________ panyanja (tsindwi, namondwe). 3 Nkhanga zidagwidwa ndi _________ (tsindwi, nkhandwe).
115
MUTU 19
thw
ndwe nkhu mphi kho pha
thw thwe thwa
thwi
kuthwa
thwanima
thwetsa
thwanithwani
116
Nyengo yadzinja
Inali nyengo yadzinja. Kumwamba kunali thwanithwani. Kuthwanimaku kunabweretsa chiyembekezo cha mvula. Mvula ikagwa, zamoyo zambiri zimasangalala. Ziphaniphani zimachita thwanithwani. Usiku wina Kondwani anaona ziphaniphani zili thwanithwani. Iye anachita chidwi ndi kuthwanimaku. Anayitana m’bale wake Mwayi. Mwayi anali chithwango mu banja la a Bengo. Iye atabwera, anachitanso 117
chidwi ndi kuthwanimako. Mwayi anati ziphaniphani zinalengedwa kuti zizithwanima.
Ntchito
A Mafunso
1 Kodi m’bale wake wa Kondwani anali yani? 2 Tchulani dzina la tizilombo tomwe timathwanima. 3 Zamoyo zimasangalala bwanji mvula ikagwa? B Kupeza thw m’mawu Pezani thw mu mawu awa. Chitsanzo
thwetsa
thwetsa
1 thwika 2 kuthwa 3 thwanima 118
MUTU 20 Kubwereza 1 Tchulani liwu loyamba lopezeka mu mayina a zinthu kapena zochitika zomwe zili mu mabokosiwa.
2 Tchulani maliwu a malembo kuchokera mu mabokosiwa.
mts
thw
mbw
ndw
119
3 Werengani maphatikizo otsatirawa. mtsa thwi mtsu ndwi ndwe mbwi thwa mbwe 4 Werengani mawu otsatirawa. mtsuko
mbwanda
kondwa
thwanima nkhandwe
mtsetse
mbwita
mtsitsi
thwika
tsindwi
kuthwa
chikondwerero
mbwee
thwanithwani ithwa
5 Werengani nkhani yotsatirayi. Mtsikana wolimba mtima
Gogo Mbwanda adali ndi mdzukulu wawo. Dzina lake lidali Takondwa. Gogoyu adapatsa Takondwa mtsuko. Iye adakondwera nawo mtsukowo. Takondwa adali mtsikana wolimba mtima. Tsiku lina adapita ku mtsinje kukatunga 120
madzi. Iye adatenganso chikwanje chakuthwa kuti akadulire nzimbe. Panjira Takondwa adaona nkhandwe. Nkhandweyo idamuopseza. Iye adatula pansi mtsukowo. Adaponya chikwanje kuti adziteteze. Iye adambwita. Mwamwayi nkhandweyo idathawa.
Ntchito Mafunso
1 Kodi mdzukulu wa Gogo Mbwanda adali yani? 2 Tchulani nyama yomwe mdzukulu wa Gogoyu adakumana nayo panjira. 3 Mukuganiza chikadachitika ndi chiyani Takondwa akadapanda kuponya chikwanje?
121
MUTU 21
thy
mbwa nji ndwe wo mtsu
thy thyo thyu thyi thya thye thyakula
thyola
thyakuka
thyoka
122
thyuka
Yohane aphika nsima
Amayi adauza Yohane kuti aphike nsima. Iye adali asadaphikepo. Yohane adathyola nkhuni zoti aphikire nsimayo. Asadayambe kuphika adakambirana ndi amayi ake motere. Amayi
: Yohane uphike nsima.
Yohane : Chabwino amayi, ndiphika. 123
Amayi
: Uphiketu nsima yothyakuka.
Amayi
: Usamale pothyakula kuti mthiko usathyoke.
Yohane : Inde amayi ndiyesetsa kuthyakula.
Yohane : Chabwino amayi. Yohane adaphika nsima. Banja lonse lidakondwera litadya nsima yothyakuka.
Ntchito
A Mafunso
1 Kodi amayi adauza Yohane kuti aphike chiyani? 2 Ndi chifukwa chiyani banja lonse lidakondwera? 3 Mukuganiza kuti ndi bwino kuti anyamata aziphika?
124
B Mawu otsutsana m’matanthauzo Pezani mawu mu B otsutsana m’matanthauzo ndi omwe ali mu A. Chitsanzo A
B
A
B
pita
bwera
inde
abambo
amayi
kwiya
kondwa
bwera
pita
ayi
125
MUTU 22
tsw
thyo nsi ntha ndwe phu
tsw tswe tswere
tswi
tswa
katswiri
tswayitswayi
126
Thandizo apita kosaka
Thandizo adali wokonda kudya zatswayitswayi. Iye adali katswiri pa uzimba. Thandizo sankaphonya polasa nyama. Tsiku lina iye adapita kuphiri kukasaka nyama. Akusaka adaona udzu ukugwedera. Thandizo adayenda monyang’ama. 127
Atapenyetsetsa adaona kalulu. Iye adaponya chibonga. Kalulu adachiona chibongacho. Iye adangoti tswere patchire. Thandizo adadziwa kuti sakadyera zatswayitswayi.
Ntchito
A Mafunso
1 Kodi Thandizo amakonda kudya zotani? 2 Kodi Thandizo ataona udzu ukugwedera adayenda motani? 3 Mukuganiza kuti kuipa kopha nyama zam’tchire mwachisawawa ndi kotani?
128
B Kupanga mawu Pangani mawu kuchokera ku malembo omwe ali mu mabokosiwa. Chitsanzo
yitswa tswayi
1
2
3
tswayitswayi
k a r i t s w i
________
l u k a l u
________
r e t s w e
________ 129
MUTU 23 ngo
msw tswe
ng’a
dzu
msw mswe mswachi
mswa mswera
mswankhono
130
mswi
phi
Kusamalira mano
Dzulo aphunzitsi anatiphunzitsa kasamalidwe ka mano. Anafotokoza kuti tizitsuka mano athu ndi mswachi. Iwo anati titha kugula mswachi kusitolo. Tithanso kupanga mswachi kuchokera ku kamtengo. Anatiphunzitsanso momwe tingapangire mswachi.
131
Patsikuli kunali mswera. Nditaweruka kusukulu, ndinakafuna kamtengo kokonzera mswachi. Ndili komweko ndinaona mbalame ya mswankhono. Mbalameyi imadya nkhono. Ndinachita mantha ndi mbalameyi komabe ndinadula kamtengoko.
Ntchito
A Mafunso
1 Kodi ophunzira anaphunzira chiyani kusukulu? 2 Kodi mbalame ya mswankhono imadya chiyani? 3 Fotokozani ubwino wosamalira mano. B Kupanga mawu Pangani mawu okhala ndi msw, tsw, nkh. Chitsanzo nkh
nkhono 132
MUTU 24
nsw
tsa mswe nkho nzi thu
nsw nswa
nswe
nswi
nswala
inswa
nswachulu
133
Ulemu athawa nswala
Tsiku lina Ulemu adapita komwe kudali chulu. Iye ankafuna kukagwira inswa. Atayandikira chulucho, adaona nyama yodabwitsa. Nyamayo inkadya masamba a mtengo wa nswachulu. Iye adathawa. 134
Ulemu adafotokozera Mayi Nswati za nyamayo. Amayiwo adati nyamayo ndi nswala. Nswala imadya masamba akunsonga zamtengo. Chifukwa cha ichi, dzina lina la nswala ndi kadyam’nsonga.
Ntchito
A Mafunso
1 Ndi chifukwa chiyani Ulemu adapita komwe kudali chulu? 2 Kodi Ulemu adaona nyama yanji? 3 Kodi inu mutaona nyama yachilendo mungatani?
135
B Kutsiriza ziganizo Tsirizani ziganizo poika nswala, Nswati, inswa kapena nswachulu m’mipata yoyenera. Chitsanzo
Ulemu adaona Mayi _____. Ulemu adaona Mayi Nswati. 1 ________ ili ndi khosi lalitali. 2 Pachulu pamatuluka _______. 3 ________ ndi dzina la mtengo.
136
MUTU 25 Kubwereza 1 Tchulani liwu loyamba lopezeka mu mayina a zinthu kapena zochitika zomwe zili mu mabokosiwa.
2 Tchulani maliwu a malembo kuchokera mu mabokosiwa.
thy
tsw
msw
nsw
137
3 Werengani maphatikizo otsatirawa. thya nswi tswe mswi mswe thyi tswa thye tswe thyo mswa nswe nswa thya tswi thyu 4 W erengani mawu otsatirawa. thyoka
nswachulu
tswere
tswii
katswiri
kathyali
mswachi
mswera
nswala
thyakula
mswankhono thyathyathya
inswa
thyapa
thyola
138
5 Werengani nkhani yotsatirayi.
A Thyolani apita kusitolo
A Thyolani adapita kusitolo yaikulu. Sitoloyi idali mu mzinda wa Mzuzu. Mwana wawo adawapempha kuti akamugulire mswachi. Mswachi wake udathyoka. Akazi awo adawauza kuti akagule ndiwo zatswayitswayi. A Thyolani atafika kusitoloko adagula mswachi ndi zipatso. Atafika pogulitsira nyama, adapeza nyama yoduladula ndi yogaya. A Thyolani adagula nyama yogaya. Atatuluka panja, adagulanso inswa. Kusitoloko adabwera dzuwa lili tswii.
139
Ntchito Mafunso
1 Kodi a Thyolani adapita kuti? 2 Tchulani zinthu zomwe a Thyolani adagula. 3 Mukuganiza chikadachitika ndi chiyani a Thyolani akadapanda kugula ndiwo?
140
MUTU 26
mpw
thyo tswi nswa chu bwe
mpw mpwa
mpwi
mpweya
141
mpwe
Mpweya Ine ndine mpweya Sindioneka kapena kugwirika Zamoyo ndi zopanda moyo zimandifuna Palibe opambana ine Ine ndine mpweya Zamoyo zimandifuna 142
Anthu, nyama ndi zomera zimandidalira Palibe opambana ine Ine ndine mpweya Kundisamalira ndimathandiza Bzalani mitengo kuti musangalale nane Pakuti palibe opambana ine.
Ntchito
A Mafunso
1 Ndani akuyankhula m’ndakatuloyi? 2 Tchulani zinthu zimene zimafuna mpweya. 3 Mukuganiza chingachitike ndi chiyani mpweya utasowa?
143
B K usiyanitsa zinthu zofuna mpweya ndi zosafuna mpweya Lembani inde ngati chinthucho chimafuna mpweya kapena ayi ngati sichifuna mpweya. Chitsanzo nswala
___
nswala
inde
1 mwala
____
2 nthiwatiwa
____
3 inswa
____
144
MUTU 27
ntch
dwe tswi mpwa nthu nso
ntch ntcha ntchu
ntche ntcho
ntchi
ntchito
ntchofu
ntchentche
ntchafu
145
Linda asirira unamwino
Linda amakhala ndi atsibweni ake a Mwale. Atsibweni akewo amagwira ntchito ya unamwino. A Mwale amagwira ntchitoyo pa chipatala cha Ntcheu. Iwo amasamalira anthu odwala matenda osiyanasiyana. Matendawa ndi monga ntchofu, edzi, kamwazi ndi malungo. 146
A Mwale amaphunzitsanso za ukhondo. Iwo amati ntchentche zimafalitsa matenda. Ntchentche zimakonda zinthu zoola. Ntchentche sizifalitsa matenda ena monga ntchofu. Linda amasirira ntchito ya unamwino.
Ntchito
A Mafunso
1 Tchulani dzina la atsibweni a Linda. 2 Kodi Linda amasirira ntchito yanji? 3 Tchulani ntchito zomwe mumasirira ndi zifukwa zake? B Kuchita sewero Chitani sewero la malonje akuchipatala pakati pa namwino ndi wodwala.
147
MUTU 28
nkhw
mwa bwe kho ntchi phu
nkhw nkhwa
nkhwi
nkhwe
nkhwenzule
nkhwazi
nkhwangwa
nkhwidzi
148
nkhwiko
Nkhwenzule yankhwidzi
Kalekale, nkhwali, nkhwazi ndi nkhwenzule zinkakhalira limodzi. Nkhwazi idali mfumu. Mbalame zonsezi zinkakhala modalirana. Patapita nthawi, nkhwenzule idayamba nkhwidzi. Tsiku lina nkhwenzule idasowetsa nkhwangwa ya nkhwali mwadala. 149
Iyo idachita izi chifukwa cha khalidwe lake. Nkhwenzule sinkakondwa ndi kupeza bwino kwa nkhwali. Poopa mlandu, nkhwenzule idathawa. Kuyambira pomwepo, nkhwenzule imapezeka usiku wokhawokha.
Ntchito
A Mafunso
1 Tchulani mayina a mbalame zitatu mu nkhaniyi. 2 Ndi chifukwa chiyani mbalame ina idasowetsa nkhwangwa? 3 Mukuganiza kuti kuipa kwa nkhwidzi ndi kotani?
150
B Ndagi/zilapi Perekani matanthauzo a ndagi/zilapi zotsatirazi. Chitsanzo
Alira atadzimenya yekha. Yankho
tambala 1 Nyumba yanga yopanda khomo. 2 Ndili ndi mphasa koma ndimagona pansi. 3 Kankhalamba aka kugwaigwa.
151
MUTU 29 ngwa
mphw dwe
wo
nzu
nkhwi
mphw mphwe
mphwa
mphwephwa
mphwi
mphwayi
mphwene
152
Mphwayi A Nyoni ankakhala m’mudzi mwa Chitumphwa. Iwo adali amphwayi ndipo ankachita zinthu mwaulesi ndi mochedwa. Nthawi zambiri, akazi awo ankachita kuwadzutsa popita kumunda. A Nyoni akadzuka, amasukusula kuchotsa mphwene. 153
Akafika kumunda, ankalima mwamphwayi. Ankabzala ndikupalira mochedwa. Banja la a Nyoni linkakolola mphwephwa zokhazokha.
Ntchito
A Mafunso
1 Tchulani dzina la munthu wamphwayi mu nkhaniyi. 2 Ndi chifukwa chiyani banja la a Nyoni linkakolola mphwephwa zokhazokha? 3 Fotokozani kuipa kwa mphwayi. B Kupanga ziganizo
Pangani ziganizo ndi mawu awa: mphwayi, mphwephwa, mwaulesi ndi palira. Chitsanzo Tamandani amalima mwaulesi.
154
MUTU 30 Kubwereza 1 Tchulani liwu loyamba lopezeka mu mayina a zinthu kapena zochitika zomwe zili mu mabokosiwa.
2 Tchulani maliwu a malembo kuchokera mu mabokosiwa.
nkhw
mphw
mpw
ntch 155
3 Werengani maphatikizo otsatirawa. mphwa
nkhwe
ntchi
nkhwa
mpwe
mphwe
ntcho
nkhwi
mpwa
ntchu
mpwi
ntcha
4 Werengani mawu otsatirawa. nkhwangwa ntchuwa
mpweya
nkhwali
mphwephwa nkhwiko
nkhwesa
ntchofu
mphwene
nkhwazi
ntchafu
nkhwidzi
ntchentche mpweche mphwayi
nkhwere
nkhwenzule ntchito
156
5 Werengani ndakatulo yotsatirayi. Mlenje wankhuli
Onani mlenje wankhuli Iye sanyambitira mphwene Amalawirira kutchire kukasaka Kukasaka nkhwali ndi nkhanga Iye samasaka nkhwenzule ndi nkhwazi Onani mlenje wankhuli Iye sachita mphwayi posaka Posaka nyama m’nkhalango Amasaka ntchefu ndi mbawala Zankhuli zili mpweche m’nyumba mwake
Ntchito
Mafunso 1 Kodi mlenje amapita nthawi yanji kokasaka? 2 Tchulani mbalame zomwe mlenje amasaka. 3 Mukuganiza ndi chifukwa chiyani mlenje samasaka nkhwenzule ndi nkhwazi? 157
MUTU 31 mphwe
mtch nkha
tchi
nkhu
mtch mtcha mtche
mtchu mtchi
mtcho
mtchetcha
mtchona
mtchini
mtchatho
158
ngo
Matenda a mtchetcha
Upile amaphunzira pa sukulu ya Mtchanga. Abambo ake a Lomba adali mtchona. Iwo adakatchona ku dziko lakutali. Atabwerera kumudzi, adagula mtchini. Banja la a Lomba lidapindula ndi mtchiniwo. Tsiku lina, Upile ankacheza ndi abambo ake. Iye adawauza za 159
matenda omwe adaphunzira kusukulu. Matendawa amatchedwa mtchetcha. Iye adawauza bambowo kuti adafunsa mafunso ambiri. Upile adaphunzira kuti mtchetcha ndi matenda woopsa.
Ntchito
A Mafunso
1 Kodi a Lomba adagula chiyani atabwerera kumudzi? 2 Kodi Upile adaphunzira zamatenda anji? 3 Mukuganiza ndi chifukwa chiyani a Lomba adakatchona ku dziko lakutali?
160
B Kulemba lembo lalikulu
Lembani lembo lalikulu koyambira kwa chiganizo chilichonse mu ziganizo zotsatirazi. Chitsanzo
mayamiko wagula mtchini. Mayamiko wagula mtchini. 1 mtchetcha ndi matenda oopsa. 2 amayi apita ku mtchini. 3 galimoto iyi ndi ya a Mtchona.
161
MUTU 32
nthw
psa mtche
dwi
tcho
thu
nthw nthwa
thanthwe
nthwe
nthwi
phunthwa
162
Nkhalango ya Liwonde
Tsiku lina Moyenda ndi Towera ankacheza motere. Towera : Iwe Moyenda, dzulo unali kuti? Moyenda : Ndinapita ku nkhalango ya Liwonde ndi makolo anga. Towera : Munakachita chiyani? 163
Moyenda : Kukaona nyama. Ee, koma ndinaphunthwa. Towera : Kuphunthwa? Iwe sumaona? Moyenda : Ndimachita mantha ndi mikango yomwe inali pathanthwe.
Towera : Imatani pathanthwepo?
Moyenda : Akuti imafuna iziona nyama zili patali. Towera : Nyamazo imazionera pathanthwepo? Moyenda : Ee, akuti mikangoyo ikaona nyamazo imazizembera ndi kuzigwira. Towera : Ndidzapite nanenso kuti ndikaione. Moyenda : Udzapitedi. Koma uzikayenda bwino kuti usakaphunthwe.
164
Ntchito
A Mafunso
1 Kodi Moyenda anapita ndi yani ku nkhalango ya Liwonde? 2 Ndi chifukwa chiyani mikango imagona pathanthwe? 3 Kodi anthu amaioperanji mikango? B Kupeza matanthauzo a mawu Pezani matanthauzo a mawu omwe ali mu A kuchokera mu B. Chitsanzo thanthwe chimwala chachikulu A B phunthwa y enda mosafuna kuti wina akuone nkhalango chimwala chachikulu thanthwe gunda kanthu ndi phazi mwadzidzidzi zembera dera la mitengo yambiri 165
MUTU 33 nkha
mtsw phu
nso
nthwe
mtsw mtswa
mtswi
mtswatswa
166
mtswe
gwi
Mbala zigwidwa
Pa sukulu ya Msangu padali mtsikana dzina lake Melifa. Tsiku lina Melifa akupita kusukulu adamva mtswatswa. Mtswatswawo unkamvekera mu nkhalango ya sukuluyo. Melifa adadabwa nawo mtswatswawo.
167
Iye adatola miyala ndi kuponya komwe kunkachokera mtswatswawo. Miyalayo idavumbulutsa mbala zomwe zimabisa mabuku patchire. Mtswatswa udapitirira pamene mbala zinkathawa. Melifa adakuwa. Aphunzitsi ndi ophunzira adakhamukira kumaloko. Iwo adathamangitsa mbalazo ndi kuzigwira. Mbalazo adakazipereka kupolisi. Aphunzitsi adayamikira Melifa.
Ntchito
A Mafunso
1 Kodi Melifa ankaphunzira kuti? 2 Kodi mbala zidabisa chiyani patchire? 3 Fotokozani kuipa kwa kuba zipangizo zasukulu.
168
B K usankha zinthu zochita mtswatswa ndi zosachita mtswatswa Ikani mawu awa galu, anthu, mbuzi, nyumba, mkango, nkhuku, msewu ndi mitambo m’magulu a zinthu zochita mtswatswa ndi zosachita mtswatswa
Chitsanzo Zochita mtswatswa Zosachita mtswatswa galu
nyumba
1
1
2
2
3
3
169
MUTU 34 mtswa
mnkhw gwi
mve
cho
mbu
mnkhw mnkhwa
mnkhwi
mnkhwani
170
mnkhwe
Malonda a mnkhwani
A Lungu ndi munthu wotchuka mu dera lathu. Iwo amagulitsa mnkhwani. A Lungu amapikula mnkhwaniwo ku msika waukulu. Iwo amayenda khomo ndi khomo kugulitsa mnkhwaniwo. Mnkhwani womwe a Lungu amagulitsa suwonongeka msanga. 171
Iwo amatengera mnkhwani mudengu. A Lungu amaphimbira mnkhwaniwo ndi masamba anthochi. Anthu ambiri amakonda kugula mnkhwani wa a Lungu. A Lungu amatchuka ndi dzina loti a Kamnkhwani. Anthu adawapatsa dzinali chifukwa cha malonda awo.
Ntchito
A Mafunso
1 Kodi a Lungu amagulitsa chiyani? 2 Ndi chifukwa chiyani a Lungu amatchedwa a Kamnkhwani? 3 Fotokozani kufunika kwa mnkhwani.
172
B Kupanga mawu
Pangani mawu okhoza kuchokera ku malembo omwe ali mu mabokosiwa. Chitsanzo ms k
a i
1
m kh
o o
2
dz m
a i
3
d ng
u e
msika
173
MUTU 35 Kubwereza 1 Tchulani liwu loyamba lopezeka mu mayina a zinthu kapena zochitika zomwe zili mu mabokosiwa.
2 Tchulani maliwu a malembo kuchokera mu mabokosiwa.
mtch
nthw
mtsw
mnkhw
174
3 Werengani maphatikizo otsatirawa. mtchu
mnkhwa
mtchi
mtswa nthwe
mnkhwe
mtcho
mnkhwi
mtswe
mtswi
mtche
nthwa
4 Werengani mawu otsatirawa. mtchetcha
thanthwe
mtswatswa mnkhwani mtchona
mtchini
phunthwa
mtchatho
5 Werengani nkhani yotsatirayi. Mayi Gunde agula mtchini
Mayi Gunde anakhala zaka zambiri ku Zimbabwe. Iwo anali mtchona. Nthawi yomwe ankabwerera kumudzi anagula
175
mtchini wogaya chimanga. Anaika mtchiniwu pafupi ndi msika woyandikana ndi thanthwe. Tsiku lina usiku, mlonda wa pa mtchini anamva mtswatswa. Mtswatswawu unkamvekera kudimba la mnkhwani. Dimbali linali pafupi ndi mtchiniwo. Atasuzumira anaona munthu. Iye anaganiza kuti anali wakuba ndipo anakuwa. Anthu anagwira munthuyo ndi kupita naye kupolisi.
Ntchito Mafunso
1 Kodi Mayi Gunde anakhala zaka zingati ku Zimbabwe? 2 Tchulani malo omwe Mayi Gunde anaika mtchini wawo. 3 Ndi chifukwa chiyani anthu anamuganizira munthuyo kuti anali wakuba? 176